19. Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao.
20. Atumiza mau ace nawaciritsa,Nawapulumutsa ku cionongeko cao.
21. Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
22. Ndipo apereke nsembe zaciyamiko,Nafotokozere nchito zace ndi kupfuula mokondwera.
23. Iwo akutsikira kunyanja nalowa m'zombo,Akucita nchito zao pa madzi akuru;
24. Iwowa apenya nchito za Yehova,Ndi zodabwiza zace m'madzi ozama.
25. Popeza anena, nautsa namondwe,Amene autsa mafunde ace.