1. Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino;Pakuti cifundo cace ncosatha.
2. Atere oomboledwa a Yehova,Amene anawaombola m'dzanja la wosautsa;
3. Nawasokolotsa kumaiko,Kucokera kum'mawa ndi kumadzulo,Kumpoto ndi kunyanja.
4. Anasokera m'cipululu, m'njira yopanda anthu;Osapeza mudzi wokhalamo.