6. Inu mbeu za Abrahamu, mtumiki wace,Inu ana a Yakobo, osankhika ace.
7. Iye ndiye Yehova, Mulungu wathu;Maweruzo ace akhala pa dziko lonse lapansi.
8. Akumbukila cipangano cace kosatha,Mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;
9. Cipanganoco anapangana ndi Abrahamu,Ndi lumbiro lace ndi Isake;
10. Ndipo anaciimikira Yakobo, cikhale malemba,Cikhale cipangano cosatha kwa Israyeli.
11. Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani,Gawo la colandira cako;
12. Pokhala iwo anthu owerengeka,Inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;
13. Nayendayenda kucokera mtundu wina kufikira mtundu wina,Kucokera ufumu wina kufikira anthu ena.
14. Sanalola munthu awasautse;Ndipo anadzudzula mafumu cifukwa ca iwowa;