14. Sanalola munthu awasautse;Ndipo anadzudzula mafumu cifukwa ca iwowa;
15. Ndi kuti musamakhudza odzozedwa anga,Musamacitira coipa aneneri anga.
16. Ndipo anaitana njala igwere dziko;Anatyola mcirikizo wonse wa mkate.
17. Anawatsogozeratu munthu;Anamgulitsa Yosefe akhale kapolo:
18. Anapweteka miyendo yace ndi matangadza;Anamgoneka m'unyolo;
19. Kufikira nyengo yakucitika maneno ace;Mau a Yehova anamuyesa.
20. Mfumuyo anatuma munthu nammasula;Woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira.
21. Anamuika akhale woyang'anira nyumba yace,Ndi woweruza wa pa zace zonse:
22. Amange nduna zace iye mwini,Alangize akulu ace adziwe nzeru.