22. Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu,Ndi maufumu kuti atumikire Yehova.
23. Iye analanda mphamvu yanga panjira;Anacepsa masiku anga.
24. Ndinati, Mulungu wanga, musandicotse pakati pa masiku anga:Zaka zanu zikhalira m'mibadwo mibadwo.
25. Munakhazika dziko lapansi kalelo;Ndipo zakumwamba ndizo nchito ya manja anu.
26. Zidzatha izi, koma Inu mukhala:Inde, zidzatha zonse ngati cabvala;Mudzazisintha ngati maraya, ndipo zidzasinthika:
27. Koma Inu ndinu yemweyo,Ndi zaka zanu sizifikira kutha.
28. Ana a atumiki anu adzakhalitsa,Ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.