2. Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga;Mundichereze khutu lanu;Tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga,
3. Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi,Ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.
4. Mtima wanga ukunga udzu wamweta, nufota;Popeza ndiiwala kudya mkate wanga.
5. Cifukwa ca liu la kubuula kwangaMnofu wanga umamatika ku mafupa anga.
6. Ndikunga bvuwo m'cipululu;Ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.
7. Ndidikira, ndikhala ngati mbawaIri yokha pamwamba pa tsindwi.
8. Adani anga anditonza tsiku lonse;Akundiyarukirawo alumbirira ine.
9. Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate,Ndi kusanganiza-comwera canga ndi misozi,
10. Cifukwa ca ukali wanu ndi kuzaza kwanu;Popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa.
11. Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali;Ndipo ine ndauma ngati udzu.
12. Koma Inu, Yehova, mukhalabe ku nthawi yonse;Ndi cikumbukilo canu ku mibadwo mibadwo.
13. Inu mudzauka, ndi kucitira nsoni Ziyoni;Popeza yafika nyengo yakumcitira cifundo, nyengo yoikika.