17. Anasamalira pemphero la iwo akusowa konse,Osapepula pemphero lao.
18. Ici adzacilembera mbadwo ukudza;Ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.
19. Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ace opatulika;Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi;
20. Kuti amve kubuula kwa wandende;Namasule ana a imfa,
21. Kuti anthu alalikire dzina la Yehova m'Ziyoni,Ndi cilemekezo cace m'Yerusalemu;