2. Ndidzacita mwanzeru m'njira yangwiro;Mudzandidzera liti?Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
3. Sindidzaika cinthu coipa pamaso panga;Cocita iwo akupatuka padera cindiipira;Sicidzandimamatira.
4. Mtima wopulukira udzandicokera;Sindidzadziwana naye woipa.
5. Wakuneneza mnzace m'tseri ndidzamdula;Wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
6. Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine;Iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.