14. Mwapenya; pakuti mumayang'anira cibvutitso ndi cisoni kuti acipereke m'manja mwanu;Waumphawi adzipereka kwa Inu;Wamasiye mumakhala mthandizi wace.
15. Thyolani mkono wa woipa;Ndipo wocimwa, mutsate coipa cace kufikira simucipezanso cina.
16. Yehova ndiye Mfumu ku nthawi yamuyaya;Aonongeka amitundu m'dziko lace.
17. Yehova, mwamva cikhumbo ca ozunzika:Mudzakhazikitsa mtima wao, mudzachereza khutu lanu:
18. Kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi,Kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa.