5. Cipangano canga cinali naye ca moyo ndi ca mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa cifukwa ca dzina langa.
6. Cilamulo ca zoona cinali m'kamwa mwace, ndi cosalungama sicinapezeka m'milomo mwace; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu,
7. Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga cidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna cilamulo pakamwa pace; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.
8. Koma inu mwapambuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'cilamulo; mwaipsa cipangano ca Levi, ati Yehova wa makamu.
9. Cifukwa cace Inenso ndakuikani onyozeka ndi ocepseka kwa anthu onse, popeza simunasunga njira zanga, koma munaweruza mwankhope pocita cilamulo.