Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi ciani? Ndi ici cakuti munena, Yense wakucita coipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa ciweruzo?