kapena munthu akakhudza ciri conse codetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa coweta codetsa, kapena mtembo wa cokwawa codetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi woparamula.