Ndipo copereka cace cikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda cirema pamaso pa Yehova.