Koma cifukwa ca iwo ndidzawakumbukila pangano la makolo ao, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.