Munthu ali yense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo ali yense wokhudza cinthu codetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;