28. Koma musamaipha ng'ombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wace tsiku limodzimodzi.
29. Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike.
30. Idyedwe tsiku lomwelo; musamasiyako kufikira m'mawa; Ine ndine Yehova.
31. Potero muwasunge malamulo anga, ndi kuwacita; Ine ndine Yehova.
32. Musamaipsa dzina langa loyera; koma ndikhale woyera pakati pa ana a Israyeli; Ine ndine Yehova wakukupatulani,
33. amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova.