Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wocotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera ku nyumba ya atate wace, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wace; koma mlendo asamadyako.