11. Munthu akagona naye mkazi wa atate wace, wabvula atate wace; awaphe ndithu onse awiri; mwazi wao ukhale pamtu pao.
12. Munthu akagona ndi mpongozi wace, awaphe onse awiri; acita cisokonezo; mwazi wao ukhale pamtu pao.
13. Munthu akagonana ndi mwamuna mnzace, monga amagonana ndi mkazi, acita conyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.
14. Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wace cocititsa manyazi ici; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale cocititsa manyazico pakati pa inu.
15. Mwamuna akagona ndi nyama amuphe ndithu; muiphenso nyamayi.
16. Mkazi akasendera kwa nyama iri yonse kugonana nayo, umuphe mkaziyo, ndi nyama yomwe; muwaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.
17. Munthu akatenga mlongo wace, mwana wamkazi wa atate wace, kapena mwana wamkazi wa mai wace, nakaona thupi lace, ndi mlongoyo akaona thupi lace; cocititsa manyazi ici; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anabvula mlongo wace; asenze mphulupulu yace.
18. Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakambvula, anabvula kasupe wace, ndi iye mwini anabvula kasupe wa nthenda yace; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao.