1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2. Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.
3. Ali yense aopemai wace, ndi atate wace; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
4. Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
5. Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.
6. Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwace muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lacitatu, muzikatentha ndi moto.