12. Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wace kufikira mapazi ace, monga momwe apenyera wansembe;
13. pamenepo wansembe aone, ndipo taonani, ngati khate lakuta thupi lace, amuche woyera wanthendayo; patuwa ponsepo; ndiye woyera.
14. Koma tsiku liri lonse ukaoneka pa iye mnofu wofiira, adzakhala wodetsedwa,
15. Ndipo wansembe aone mnofu wofiirawo, namuche wodetsedwa; mnofu wofiira ndiwo wodetsa; ndilo khate.
16. Kapena mnofu wofiira ukasandukanso, nusandulika wotuwa, afike kwa wansembe,
17. ndi wansembe amuone, ndipo taonani, ngati nthenda yasandulika yotuwa, wansembe amuche woyera wanthendayo; ndiye woyera.