Ndipo Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwacotse pakhomo pa malo opatulika kumka nao kunja kwa cigono.