Efraimu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse acurukitsa mabodza ndi cipasuko, ndipo acita pangano ndi Asuri, natenga mafuta kumka nao ku Aigupto,