Ndidzakusiya bwanji, Efraimu? ndidzakupereka bwanji, Israyeli? ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zacifundo zanga zilira zonse pamodzi.