1. Ndipo Yakobo anaitana ana ace amuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu cimene cidzakugwerani inu masiku akudzawo.
2. Sonkhanani, tamvani, ana amuna a Yakobo:Tamverani Israyeli atate wanu:
3. Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi ciyambi ca mphamvu yanga;Ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.
4. Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana;Cifukwa unakwera pa kama wa atate wako;Pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
5. Simeoni ndi Levi ndiwo abale;Zida za mphulupulu ndizo malupanga ao.
6. Mtima wangawe, usalowe mu ciungwe cao;Ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano ao;Cifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu,M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.
7. Kutembereredwekukwiyakwao, cifukwa kunali koopsya;Ndi kupsya mtima kwao, cifukwa kunali kwankharwe;Ndidzawagawanitsa m'YakoboNdidzabalalitsa iwo m'Israyeli.
8. Yuda, abale ako adzakuyamika iwe;Dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako;Ana amuna a atate wako adzakuweramira.