Ndipo panali m'mamawa mtima wace unabvutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a m'Aigupto, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lace; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.