Ndipo pamene dziko lonse la Aigupto linali ndi njala, anthu anapfuulira Farao awapatse cakudya; ndipo Farao anati kwa Aaigupto onse, Pitani kwa Yosefe: cimene iye anena kwa inu citani.