Woyang'anira m'kaidi sanayang'anira kanthu kali konse kamene kanali m'manja a Yosefe, cifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazicita, Yehova anazipindulitsa.