25. ana amuna a Biliha mdzakazi wace wa Rakele: ndiwo Dani ndi Nafitali;
26. ndipo ana amuna a Zilipa mdzakazi wace wa Leya: ndiwo Gadi ndi Aseri: amenewo ndi ana amuna a Yakobo amene anabala iye m'Padanaramu.
27. Ndipo Yakobo anafika kwa Isake atate wace ku Mamre, ku KiriyatiAriba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isake.
28. Ndipo masiku a Isake anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu.
29. Ndipo Isake anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wace, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ace amuna anamuika iye.