Ndipo pakumva ico ana ace amuna a Yakobo anabwera pocokera kudambo: amunawo ndipo anaphwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, cifukwa iyeyo anacita copusa coipira Israyeli pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndico cosayenera kucita.