Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Cifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamucha dzina lace Simeoni.