1. Ndipo Yakobo ananka ulendo wace, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa.
2. Ndipo anayang'ana, taonani, citsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pacitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa citsime unali waukuru.
3. Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa citsime pamalo pace.
4. Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? nati, Ndife a ku Harana.
5. Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wace wa Nahori? nati, Timdziwa.
6. Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wace wamkazi alinkudza nazo nkhosa.
7. Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni.