Ndipo iye anati, Kodi si ndico cifukwa anamucha dzina lace Yakobo? kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi smunandisungira ine mdalitso?