Ndipo panali atakalamba Isake, ndi maso ace anali a khungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wace wamwamuna wamkuru, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.