Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine dine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, cifukwa kuti Ine ndiri ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kucurukitsa mbeu zako, cifukwa ca Abrahamu kapolo wanga.