Ndipo Isake anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wace; cifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazicha maina monga maina omwe anazicha atate wace.