34. Ndipo anati, Ine ndine mnyamata wa Abrahamu.
35. Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo anakula kwakukuru; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golidi, ndi akapolo ndi adzakazi, oeli ngamila ndi aburu.
36. Ndipo Sara mkazi wace wa mbuyanga anambalira mbuyanga mwana wamwamuna, mkaziyo anali wokalamba; ndipo anampatsa mwanayo zonse ali nazo.