Cifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ace ndi banja lace la pambuyo pace, kuti asunge njira ya Yehova, kucita cilungamo ndi ciweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu comwe anamnenera iye.