28. ndi Obali, ndi Abimaele, ndi Sheva;
29. ndi Ofiri ndi Havila, ndi obabi; onse amenewa ndi ana a okitani.
30. Kwao kunayamba pa Mesa pakunka ku Sefere phiri la kum'mawa.
31. Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
32. Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu pa dziko lapansi, citapita cigumula.