20. Amenewa ndi ana amuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
21. Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Ebere, mkuru wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana.
22. Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Ashuri, ndi Aripakasadi, ndi Ludi, ndi Aramu.
23. Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli, ndi Getere, ndi Masi.
24. Aripakasadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Ebere.
25. Kwa Ebere ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelege; cifukwa kuti m'masiku ace dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwace ndi Yokitani.
26. Ndipo Yokitani anabala Alamodadi, ndi Selefe, ndi Hazaramaveti, ndi Yera;
27. ndi Hadorimu ndi Uzali, ndi Dikila;
28. ndi Obali, ndi Abimaele, ndi Sheva;