1. Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu, ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana amuna, citapita cigumula cija.
2. Ana amuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Mesheki, ndi Tirasi,
3. Ndi ana amuna a Gomeri: Asekenazo, ndi Rifata, ndi Togarma.
4. Ndi ana amuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu.
5. Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa cinenedwe cao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
6. Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Mizraimu, ndi Puti, ndi Kanani.
7. Ndi ana amuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedane.
8. Ndipo Kusi anabala Nimrode; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi.
9. Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: cifukwa cace kunanenedwa, Monga Nimrode mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.