28. Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwela, kuloza kumwela, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati ndi Kadesi, ku mtsinje wa Aigupto, kufikira ku nyanja yaikuru.
29. Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israyeli ndi kucita maere, likhale colowa cao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.
30. Ndipo malekezero a mudzi ndi awa: mbali ya kumpoto avese mabango zikwi zinai mphambu mazana asanu;
31. ndi zipata za mudzi zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israyeli; zipata zitatu kumpoto: cipata cimodzi ca Rubeni, cipata cimodzi ca Yuda, cipata cimodzi ca Levi;
32. ndi ku mbali ya kum'mawa zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: cipata cimodzi ca Yosefe, cipata cimodzi ca Benjamini, cipata cimodzi ca Dani;