Nutengeko mwazi wace, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pa ngondya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wace pozungulira; motero uliyeretse ndi kulicitira cotetezera.