Ndipo anadza nane ku Kacisi, nayesa nsanamira zace, kupingasa kwace mikono isanu ndi umodzi cakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi cauko, ndiko kupingasa kwa cihema cija.