Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda m'Israyeli, cigwa ca opitawo kum'mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wace wonse, nadzacicha, Cigwa ca unyinji wa Gogi.