Seba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisi, ndi misona yace yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kucoka nazo siliva ndi golidi, kucoka nazo zoweta ndi cuma, kulanda zankhondo zambiri?