Mwa kucuruka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi ciwawa, ndipo unacimwa; cifukwa cace ndinakukankha kukucotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukucotsa pakati pa miyala yamoto.