Waparamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zako zako; cifukwa cace ndakuika ukhale citonzo ca amitundu ndi coseketsa ca maiko onse.