Cifukwa cace unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzauchulanso mwambi m'Israyeli; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzacitika masomphenya ali onse.