Cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani ku mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani mucoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israyeli.