Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkuru, ku malo dzina lace Kasifiya; ndinalooganso m'kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ace Anetini, pa malo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu.